Zimbabwe

From Wikipedia
Jump to: navigation, search

Zimbabwe ndi limodzi mwa maiko a kumwera kwa Afrika ndipo dzikoli ndi lomwe kale linkalamuliridwa muchisamunda cha angerezi pomwe akalitchula kuti Rhodesia. Nsogoleri wadzikoli pakali pano ndi Robert Mugabe amene anayamba kulamulira dzikoli pamene linalanda ulamuliro kuchokera kwa angerezi m'chaka cha 1980.

Potsatira zokambirana zothetsa mapokoso ndi chipolowe chomwe chinabuka pambuyo pamasankho apa 21 Marichi, 2008 a Morgan Tshangirai omwe ndi m'tsogoleri wa chipani cha Movement for Democratic Change anakhala Nduna yaikulu ya boma.